1Patapita masiku pangʼono, Yesu atalowanso mu Kaperenawo, zinamveka kuti wabwera ali mʼnyumba. 2Choncho anthu ambiri anasonkhana kotero kuti panalibenso malo, ngakhale ndi pa khomo pomwe, ndipo Iye anawalalikira mawu. 3Amuna anayi anabwera, atanyamula munthu wofa ziwalo. 4Popeza sakanatha kufika naye kwa Yesu chifukwa cha gulu la anthu, anasasula denga chapamwamba pamene panali Yesu, ndipo atabowoleza, anatsitsa mphasa yomwe munthu wofa ziwaloyo anagonapo.